Kusiyana kwa AMAYI A CHISILAMU ndi Amayi a mu Chikhalidwe cha Chiyuda ndi Chikhristu

Chewa — Chicheŵa / Chinyanja

Kusiyana kwa AMAYI A CHISILAMU ndi Amayi a mu Chikhalidwe cha Chiyuda ndi Chikhristu

Ndikufuna kutsindika kumayambiliro kwa bukuli kuti cholinga changa polemba mutu umenewu sikuzembera Chiyuda kapena Chikhristu. Monga Asilamu, timakhulupilira kuti ziwirizi zinachokera kwa Mulungu pachiyambi, ndipo palibe amene angakhale Msilamu popanda kukhulupilira Mose ndi Yesu monga Aneneri akuluakulu a Mulungu. Ndikufuna kutsimikiza kuti Chisilamu ndi uthenga woona kuyambira kale mpaka lero lino, komanso ndi uthenga womaliza womwe watsala wochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu. Choncho, ndaima kwambiri pakulongosola mmene zipembedzo zitatuzi (Chiyuda, Chikhristu ndi Chisilamu) zimawaonera akazi, osati momwe zimaonekera ndi myandamyanda yomwe ikutsata za dziko lapansi. Nchifukwa chake ndikugwiritsa ntchito maumboni ambiri kuchokera mu Qur’an, mawu a Mtumiki Muhammad salla Allah alaih wasallam, Baibulo, Talmud, ndi mawu a Atsogoleri azipembedzo amphamvu kwambiri, omwe maganizo awo athandizira kwambiri pakufotokoza Chikhristu. Kukhala ndi chidwi pa kufufuza kuchokera mmaumboni oterewa kukuthandiza kudziwa kuti kuchimvetsetsa chipembedzo kuchokera mu zikhalidwe za ongotsatira chabe ndikosocheretsa. Anthu ambiri amasokoneza chikhalidwe ndi chipembedzo, ndipo ambiri sadziwa zomwe mabuku awo achipembedzo akunena, komanso ena ambiri salabada zimenezo. Wolemba Dr. Sherif Abdel Azeem.

download icon